ANTHU OFUNA KUBA NJINGA YA KABAZA APHEDWA

by wongani Chipeta

Anyamata amene amafuna kuba njinga ya kabaza aphedwa kwa Goliati m’boma la Thyolo .

Anyamatawa anagwidwa ndi anthu pomwe amafuna kuba njinga ya mkulu wina wochita kabaza.Anthuwa atawagwira anakawatsekera ku polisi ya Goliati m’boma lomwelo.

Koma kamba kosakhutira anthu okwiya anapita ku polisiko ndi kuthyola chipinda chosungirako anthu ogwidwa kamba kowaganizira milandu ndi kutulutsa mbavazo.

Anthuwo kenako anapha akubawo ndi miyala. Nthawiyi nkuti apolisi anali atathawa udindo wopulumutsa mbavazo chifukwa cha mkwiyo wa anthu.

Chenjezo: zithuzi zoopsa mmusimu!

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *