ACHINYAMATA AKWIYA NDI ZOMWE BOMA LACHITA

olemba: Dr Mwale

Achinyamata ambiri mdziko muno ndi okhudzidwa ndi zomwe boma la Tonse Alliance lachita pobwezeretsa anthu ena omwe anapuma ntchito kuti ayambenso kugwirantchito.

Dzulo kwatuluka chikalata chimene chaonetsa kusintha ma udindo a anthu ena monga ma principle secretaries. mchikalatachi mukuonetsa anthu awiri omwe anapuma pa ntchito koma boma lawaitanaso kuti ayambenso kugwira ntchito. anthuwa ndi Mr Chilabade, omwe ali ku Human Resource Department komano Mr maweru omwe apita ku irrigation.

Nthawi ya campaign a Chakwera ndi achilima analalikira dziko lonse kusaka vote ndi uthenga oti azalemba ntchito achinyamata omwe akungokhala,ndipo azakweza anthu mmaudindo.
Anthu anakhulupirira anthu awiriwa ndipo anawapatsa vote ndichiyembekezo kuti ntchito zisamasowe mdziko muno.

Komatu nkhani ili apa lero ndiyosiyana ndi zomwe awiriwa analonjeza, iwo sanafune kulemba anthu ena ntchito koma kukangotenga anthu omwe anapuma kale pantchito kuyamba kugwirantchito ntchito pomwe ena ma certicate awo akungoola mnyumba kusowa kolowera.

Zimene apanga apapa ndikuwauza achinyamata akumalawi kuti

(1) alibe maphunziro okwanira.

(2) alibe experience

(3) nthawi yawo sinakwane.

Inde mwina ntchito 1 million zikubwera koma zomwe mwapanga apa muwafotokozera bwanji achinyamata omwe anakuvoterani mwa unyinji podana ndi ulamuliro wa agogo?

Munthu akudya za penshion komanso azilandilanso salary pomwe ena ulova wavuta zikukumvekerani bwanji?

Boma liganizepo bwino ndipo ngati kuli koyenera anthuwa achotsedwe ndipo a chinyamata ena omwe ali kale mu ma department amenewo atengedwe ndipo mmalo mwawo ena alembedwe ntchito ndi khukulupira munalonjeza kuti muzizamva madandaulo a anthu.

Uno ndi mwezi wa chiwiri Tonse alliance chitengereni boma ndipo ife lonjezo lomwe tinasunga ndi ntchito 1 million mu Chaka choyamba apa kwatsala miyezi 10

Anyamata kukambisana za tsogolo lawo
Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *